7 Popeza zipangizo zinakwanira nchito yonse icitike, zinatsalakonso.
8 Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akucita nchitoyi anapanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi; ndi lofiira, ndi lofiira, ndi akerubi, nchito ya mmisiri.
9 Utali wace wa nsaru yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi mikono inai; nsaru zonse zinafanana muyeso wao.
10 Ndipo analumikiza nsaru zisanu yina ndi inzace; nalumikiza nsaru zisanu zina yina ndi inzace.
11 Ndipo anaika magango ansaru yamadzi m'mphepete mwace mwa nsaru imodzi ku mkawo wa cilumikizano; nacita momwemo m'mphepete mwace mwa nsaru ya kuthungo, ya cilumikizano caciwiri.
12 Anaika magango makumi asanu pa nsaru imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; magango anakomanizana lina ndi linzace.
13 Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolidi, namanga nsaru pamodzi ndi zokowerazo; ndipo kacisi anakhala mmodzi.