13 Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
14 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite,
15 Muka kwa Farao m'mawa; taona, aturuka kumka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.
16 Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumukire m'cipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano.
17 Atero Yehova, Ndi ici udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo iri m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.
18 Ndi nsomba ziri m'nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aaigupto adzacita mtima useru ndi kumwa madzi a m'nyanjamo.
19 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m'Aigupto, pa nyanja yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Aigupto, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala.