41 owerengedwa ao a pfuko la Aseri, ndiwo zikwi makumi anai mphambu cimodzi kudza mazana asanu.
42 A ana a Nafitali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo;
43 owerengedwa ao a pfuko la Nafitali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.
44 Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israyeli, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lace.
45 Potero owerengedwa onse a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli;
46 inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.
47 Koma Alevi monga mwa pfuko la makolo ao sanawerengedwa mwa iwo.