50 koma iwe, uike Alevi asunge kacisi wa mboni, ndi zipangizo zace zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula kacisi, ndi zipangizo zace zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa kacisi.
51 Ndipo akati amuke naye kacisiyo, Aleviamgwetse, ndipo akati ammange, Alevi amuimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe,
52 Ndipo ana a Israyeli amange mahema ao, yense ku cigono cace, ndi yense ku mbendera yace, monga mwa makamu ao.
53 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa kacisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israyeli; ndipo Alevi azidikira kacisi wa mboni.
54 Momwemo ana a Israyeli anacita monga mwa zonse Yehova adauza Mosel anacita momwemo.