4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriamu modzidzimutsa, Turukani inu atatu kudza ku cihema cokomanako. Pamenepo anaturuka atatuwo.
5 Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la cihema, naitana Aroni ndi Miriamu; naturuka onse awiri.
6 Ndipo anati, Tamvani tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.
7 Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.
8 Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, maonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.
9 Pamenepo Mulungu anawapsera mtima iwo; nawacokera iye.
10 Ndipo mtambo unacoka pacihema; ndipo taonani, Miriamu anali wakhate, wa mbu ngati cipale cofewa; ndipo Aroni anapenya Miriamu, taonani, anali wakhate.