1 Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya nchito yanu ya nsembe.
2 Ndiponso abale ako, pfuko la Alevi, pfuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la cihema ca mboni.
3 Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa cihema conse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.
4 Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa cihema cokomanako, kucita nchito yonse ya cihema; koma mlendo asayandikize inu.
5 Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israyeli.