8 Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israyeli; cifukwa ca kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.
9 Izi ndi zako pa zinthu zopatulikitsa, zosafika kumoto; zopereka: zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zaucimo, ndi nsembe zao zonse zoparamula, zimene Andibwezera Ine, zikhale zopatulikitsa za iwe ndi za ana ako amuna.
10 Muzizidya izi monga zopatulikitsa; mwamuna yense adyeko; uziyese zopatulika.
11 Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israyeli; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko.
12 Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa, zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.
13 Zipatso zoyamba zonse ziri m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.
14 Ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zako.