4 Ndipo anayenda ulendo kucokera ku phiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada cifukwa ca njirayo.
5 Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kuticotsa ku Aigupto kuti tifere m'cipululu? pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wacabe uwu.
6 Pamenepo Yehova anatumiza njoka zamoto pakati pa anthu, ndipo zinaluma anthu; nafapo anthu ambiri a Israyeli.
7 Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tacimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti aticotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu.
8 Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Upange njoka yamoto; nulike pa mtengowace; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo.
9 Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu ali yense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo.
10 Pamenepo ana a Israyeli anayenda ulendo, namanga mahema m'Oboti.