1 Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israyeli, sanamuka, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yace kucipululu.
2 Ndipo Balamu anakweza maso ace, naona Israyeli alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.
3 Pamenepo ananena fanizo lace, nati,Balamu mwana wa Beori anenetsa,Ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;
4 Wakumva mau a Mulungu anenetsa,Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,Wakugwa pansi maso ace openyuka:
5 Ha! mahema ako ngokoma, Yakobo;Zokhalamo zako, Israyeli!
6 Ziyalika monga zigwa,Monga minda m'mphepete mwanyanja,Monga khonje waoka Yehova,Monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.
7 Madzi adzayenda naturuka m'zotungira zace,Ndi mbeu zace zidzakhala ku madzi ambiri,Ndi mfumu yace idzamveka koposa Agagi,Ndi ufumu wace udzamveketsa.