12 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,
13 Cinkana Balaki akandipatsa nyumba yace yodzala ndi siliva ndi golidi, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kucita cokoma kapena coipa ine mwini wace; conena Yehova ndico ndidzanena ine?
14 Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzacitira anthu anu, masiku otsiriza.
15 Ndipo ananena fanizo lace, nati,Balamu mwana wa Beori anenetsa,Ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;
16 Anenetsa wakumva mau a Mulungu,Ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba,Wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,Wakugwa pansi wopenyuka maso;
17 Ndimuona, koma tsopano ai; Ndimpenya, koma si pafupi ai;Idzaturuka nyenyezi m'Yakobo,Ndi ndodo yacifumu idzauka m'Israyeli,Nidzakantha malire a Moabu,Nidzapasula ana onse a Seti,
18 Ndi Edomu adzakhala ace ace,Seiri lomwe lidzakhala lace lace, ndiwo adani ace;