19 Koma Israyeli adzacita zamphamvu.Ndipo wina woturuka m'Yakobo adzacita ufumu;Nadzapasula otsalira m'mudzi.
20 Ndipo anayang'ana ku Amaleki, nanena fanizo lace, nati,Amaleki ndiye woyamba wa amitundu;Koma citsiriziro cace, adzaonongeka ku nthawi zonse.
21 Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lace, nati,Kwanu nkokhazikika,Wamanga cisa cako m'thanthwe.
22 Koma Kaini adzaonongeka,Kufikira Asuri adzakumanga nsinga.
23 Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ha! adzakhala ndi moyo ndani pakucita ici Mulungu?
24 Koma zombo zidzafika kucokera ku doko la Kitimu,Ndipo adzasautsa Asuri, nadzasautsa Ebere,Koma iyenso adzaonongeka.
25 Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwace; ndi Balaki yemwe anamka njira yace.