1 Ndipo Israyeli anakhala m'Sitimu, ndipo anthu anayamba kucita cigololo ndi ana akazi a Moabu;
2 popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.
3 Pamene Israyeli anaphatikana ndi Baala Peori, Mulungu anapsa mtima pa Israyeli.
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akuru onse a anthu nuwapacikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova ucoke kwa Israyeli.