1 Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati,
2 Werenga khamu lonse la ana a Israyeli, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akuturukira kunkhondo m'Israyeli.
3 Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Moabu pa Yordano kufupi ku Yeriko, ndi kuti,
4 Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israyeli, amene adaturuka m'dziko la Aigupto.