4 Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israyeli, amene adaturuka m'dziko la Aigupto.
5 Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israyeli; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;
6 Hezeroni, ndiye kholo la banja la Ahezeroni; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.
7 Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu,
8 Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.
9 Ndi ana a Eliyabu: Nemueli, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, mula anatsutsana ndi Yehova;
10 ndipo dziko linayasama pakamwa pace, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja mote unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo cizindikilo.