2 Uza ana a Israyeli, nuti nao, Muzisamalira kubwera naco kwa Ine copereka canga, cakudya canga ca nsembe zanga zamoto, ca pfungo lokoma, pa nyengo yace yoikika.
3 Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: ana a nkhosa awiri a caka cimodzi opanda cirema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.
4 Mwana wa nkhosa mmodziyo umpereke m'mawa, ndi mwana wa nkhosa winayo umpereke madzulo;
5 ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la bini wa mafuta opera.
6 Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika ku phiri la Sinai, icite pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
7 Ndi nsembe yace yothira ya mwana wa nkhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la bini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya cakumwa colimba.
8 Ndi mwana wa nkhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yace, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.