20 ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo;
21 upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi; uzitero ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;
22 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo, yakutetezera inu.
23 Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza ya m'mawa, ndiyo ya nsembe yopsereza kosalekeza.
24 Momwemo mupereke cakudya ca nsembe yamoto ca pfungo lokoma la Yehova, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiri, cakupereka pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.
25 Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.
26 Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'madyerero anu a masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.