1 Ndipo mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.
2 Pamenepo muzipereka nsembeyopsereza ya pfungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi opanda cirema;
3 ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo,
4 ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri;
5 ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo, yakutetezera inu;