32 Ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri ng'ombe zisanu ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;
33 ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
34 ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.
35 Tsiku lacisanu ndi citatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamacita nchito ya masiku ena;
36 koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri, a caka cimodzi, opanda cirema;
37 nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;
38 ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.