41 Ndipo unditengere Ine Alevi (ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israyeli.
42 Ndipo Mose anawawerenga, monga Yehova adamuuza, oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli.
43 Ndipo amuna onse oyamba kubadwa, powerenga maina, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri mphambu atatu.
44 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
45 Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova.
46 Kunena za mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza atatuwo oyamba kubadwa a ana a Israyeli, akuposa Alevi, akaomboledwe,
47 ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri);