23 zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.
24 Ndipo muzitsuke zobvala zanu tsiku lacisanu ndi ciwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m'cigono.
25 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
26 Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe; ndi Eleazara wansembe, ndi akuru a nyumba za makolo za khamulo;
27 nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anaturuka kunkhondo, ndi khamu lonse.
28 Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akuturuka kunkhondo apereke kwa Yehova; munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.
29 Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.