1 Maulendo a ana a Israyeli amene anaturuka m'dziko la Aigupto monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.
2 Ndipo Mose analembera maturukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa maturukidwe ao.
3 Ndipo anacokera ku Ramese mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi woyamba; atacita Paskha m'mawa mwace ana a Israyeli, anaturuka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aaigupto onse,
4 pamene Aaigupto ailalikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.
5 Ndipo ana a Israyeli macokera ku Ramese, nayenda namanga ku Sukoti.
6 Nacokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a cipululu.
7 Ndipo anacokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwace kwa Baala Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.