25 ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere ku mudzi wace wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.
26 Koma wakupha munthu akaturuka nthawi iri yonse kulumpha malire a mudzi wace wopulumukirako kumene anathawirako;
27 nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mudzi wace wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kucimwira mwazi;
28 popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wace wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lace lace.
29 Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la ciweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.
30 Ali yense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.
31 Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, naparamula imfa; koma aziphedwa ndithu.