1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
2 Werengani ana a Kohati pakati pa ana a Levi, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,
3 kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire nchito ya cihema cokomanako.
4 Nchito ya ana a Kohati m'cihema cokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulikitsa:
5 akati amuke a m'cigono, Aroni ndi ana ace amuna azilowa, natsitse nsaru yocinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,
6 ndi kuikapo cophimba ca zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsaru yamadzi yeni yeni, ndi kupisako mphiko zace.