4 Nchito ya ana a Kohati m'cihema cokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulikitsa:
5 akati amuke a m'cigono, Aroni ndi ana ace amuna azilowa, natsitse nsaru yocinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,
6 ndi kuikapo cophimba ca zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsaru yamadzi yeni yeni, ndi kupisako mphiko zace.
7 Ndi pa gome la mkate waonekera ayale nsaru yamadzi, naikepo mbale zace, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa cikhalire uzikhalaponso.
8 Ndipo ayale pa izi nsaru yofiira, ndi kuliphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.
9 Ndipo atenge nsaru yamadzi, ndi kuphimba coikapo nyali younikira, ndi nyali zace, ndi mbano zace, ndi zaolera zace, ndi zotengera zace zonse za mafuta zogwira nazo nchito yace.
10 Ndipo acimange ndi cipangizo zace zonse m'cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa conyamulira.