12 Wakubwera naco copereka cace tsiku loyamba ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu, wa pfuko la Yuda:
13 copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembeyaufa;
14 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
15 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
16 ronde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
17 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa: asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Nahesoni mwana wa Aminadabu.
18 Tsiku laciwiri Netaneli mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera naco cace: