14 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
15 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
16 ronde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
17 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa: asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Nahesoni mwana wa Aminadabu.
18 Tsiku laciwiri Netaneli mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera naco cace:
19 anabwera naco copereka cace mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
20 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;