44 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;
45 ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;
46 tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;
47 ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Eliyasafe mwana wa Deyueli.
48 Tsiku lacisanu ndi ciwiri kalonga wa ana a Efraimu Elisama mwana wa Amihudi:
49 copereka cace mbizi Imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
50 cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;