9 Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israyeli? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.
10 Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kucokera ku Efraimu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.
11 Nalimbika mtima Amaziya, natsogolera anthu ace, namuka ku Cigwa ca Mcere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi.
12 Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, nawakankha pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.
13 Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera midzi ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betihoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.
14 Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yace, naigwadira, naifukizira,
15 Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu?