1 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Turuka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;
2 ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukuru, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
3 ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi,
4 Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anaturuka m'Harana.
5 Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wace, ndi Loti mwana wa mphwace, ndi cuma cao cimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harana; naturuka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
6 Ndipo Abramu anapitira m'dziko kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.
7 Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.