1 Ndipo panali atakalamba Isake, ndi maso ace anali a khungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wace wamwamuna wamkuru, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.
2 Ndipo anati, Taonatu, ndakalamba, sindidziwa tsiku la kufa kwanga:
3 tsopano tengatu zida zako ndi phodo lako ndi uta wako, numuke kuthengo kundisakira ine nyama;
4 nundikonzere ine cakudya cokolera conga comwe ndicikonda ine, nudze naco kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.
5 Ndipo anamva Rebeka pamene Isake ananena ndi Esau mwana wace. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo.
6 Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wace, nati, Taona ndinamva atate wako alinkunena ndi Esau mkuru wako kuti,
7 Unditengere ine nyama, undikonzere ine cakudya cokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe.
8 Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe.
9 Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino ta mbuzi; ndikonzere nato cakudya cokolera ca atate wako conga comwe acikonda:
10 ndipo udzapita naco kwa atate wako, kuti adye, ndi kukudalitsa iwe asanafe,
11 Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amace, Taonani, Esau mkuru wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu, wosalala.
12 Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pace ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
13 Ndipo amace anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.
14 Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amace; amace ndipo anakonza cakudya cokolera conga cimene anacikonda atate wace.
15 Ndipo Rebeka anatenga zobvala zokoma za Esau, mwana wace wamkuru zinali m'nyumba, nabveka nazo Yakobo mwana wace wamng'ono;
16 ndipo anabveka zikopa za tiana tambuzi pa manja ace ndi pakhosi pace posalala;
17 ndipo anapereka m'dzanja la mwana wace Yakobo cakudya cokoleraco, ndi mikate imene anaipanga.
18 Ndipo iye analowa kwa atate wace, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?
19 Ndipo Yakobo anati kwa atate wace, Ndine Esau mwana wanu wamkuru; ndacita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.
20 Ndipo Isake anati kwa mwana wace, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Cifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.
21 Ndipo Isake anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.
22 Ndipo Yakobo anasendera kwa Isake atate wace, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau.
23 Ndipo sanazindikira iye, cifukwa kuti manja ace anali aubweya, onga manja a Esau mkuru wace; ndipo anamdalitsa iye.
24 Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? ndipo anati, Ndine amene.
25 Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.
26 Ndipo Isake atate wace anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.
27 Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zobvala zace, namdalitsa, nati,Taona, kununkhira kwa mwana wanga,Kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
28 Mlungu akupatse iwe mame a kumwamba,Ndi zonenepa za dziko lapansi,Ndi tirigu wambiri ndi vinyo;
29 Anthu akutumikire iwe,Mitundu ikuweramire iwe;Ucite ufumu pa abale ako,Ana a amako akuweramire iwe;Wotemberereka ali yense akutemberera iwe,Wodalitsika ali yense akudalitsa iwe.
30 Ndipo panali atatha Isake kumdalitsa Yakobo, ataturuka Yakobo pamaso pa Isake atate wace, Esau mkuru wace analowa kucokera kuthengo,
31 Ndipo iyenso anakonza cakudya cokolera, nadza naco kwa atate wace, nati kwa atate wace, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wace, kuti moyo wanu undidalitse ine.
32 Ndipo Isake atate wace anati kwa iye, Ndiwe yani? ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau.
33 Ndipo Isake ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukuru, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadaloweiwe, ndipondamdalitsaiye? inde, adzadalitsika.
34 Pamene Esau anamva mau a atate wace Isake, analira ndi kulira kwakukuru ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wace, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.
35 Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.
36 Ndipo iye anati, Kodi si ndico cifukwa anamucha dzina lace Yakobo? kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi smunandisungira ine mdalitso?
37 Ndipo anayankha Isake nati kwa Esau, paona, ndamuyesa iye mkuru wako, ndi abale ace onse ndampatsa iye akhale akapolo ace; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakucitira iwe ciani?
38 Ndipo Esau anati kwa atate wace, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga, Ndipo Esau anakweza mau ace nalira.
39 Ndipo Isake atate wace anayankha nati kwa iye,Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi,Mpa mame a kumwamba akudzera komwe;
40 Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wamphwako;Ndipo padzakhalapamene udzapulumuka,Udzacotsa gori lace pakhosi pako.
41 Ndipo Esau anamuda Yakobo cifukwa ca mdalitso umene atate wace anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwace, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.
42 Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wace wamkuru: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wace wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkuru wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wace kuti adzakupha iwe.
43 Ndipo tsopane mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harana;
44 ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka wamcokera ukali wa mkuru wako;
45 mpaka wakucokera mkwiyo wa mkuru wako, kuti aiwale cimene wamcitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?
46 Ndipo anati Rebeka kwa Isake, Ndalema moyo wanga cifukwa ca aria akazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana akazi a Heti, onga ana akazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?