Genesis 42 BL92

Abale a Yosefe afika ku Aigupto

1 Ndipo anaona Yakobo kuti m'Aigupto munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ace amuna, Cifukwa canji mulinkuyang'anana?

2 Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti m'Aigupto muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.

3 Ndipo abale ace a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu m'Aigupto.

4 Koma Yakobo sanamtuma Benjamini mphwace wa Yosefe, pamodzi ndi abale ace, cifukwa anati, Coipa cingamgwere iye.

5 Ndipo ana amuna a Israyeli anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.

6 Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ace a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.

7 Ndipo Yosefe anaona abale ace, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula cakudya.

8 Ndipo Yosefe anazindikira abale ace, koma iwo sanamzindikira iye.

9 Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analoto za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko.

10 Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula cakudya.

11 Tonse tiri ana amuna a munthu mmodzi; tiri oona, akapolo anu, sitiri ozonda.

12 Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.

13 Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana amuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.

14 Ndipo Yosefe anati kwa iwo, dico cimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda.

15 Mudzayesedwa ndi ici, pali moyo wa Farao, simudzaturuka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.

16 Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona ziri mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.

17 Ndipo anaika onse m'kaidi masiku atatu.

18 Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lacitatu, Citani ici, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;

19 ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m'kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu;

20 koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anacita comweco.

21 Ndipo iwo anati wina ndi mnzace, Tacimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kubvutidwa kwa mtima wace, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, cifukwa cace kubvutidwa kumene kwatifikira.

22 Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanena kwa inu kuti, Musacimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? cifukwa cacenso, taonani mwazi wace ufunidwa.

23 Ndipo sanadziwa kuti, Yosefe anamva; cifukwa anali ndi womasulira.

24 Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao.

25 Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, ali yense m'thumba mwace, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.

Abale a Yosefe apita kwao

26 Ndipo anasenzetsa aburu ao tirigu wao nacokapo.

27 Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lace kuti adyetse buru wace pacigono, anapeza ndalama zace; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lace.

28 Ndipo iye anati kwa abale ace, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, ziri kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzace kuti, Nciani ici Mulungu waticitira ife?

29 Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo;

30 kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankharwe, natiyesa ife ozonda dziko.

31 Koma ife tinati kwa iye, Tiru anthu oona; sitiri ozonda;

32 tiri abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani.

33 Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;

34 idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: comweco ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzacita malonda m'dziko muno.

35 Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lace; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa,

36 Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzacotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.

37 Ndipo Rubeni anati kwa atate wace, kuti, Muwaphe ana anga amuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.

38 Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, cifukwa kuti mkuru wace wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati coipa cikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.