Genesis 15 BL92

Mulungu apangana ndi Abramu

1 Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine cikopa cako ndi mphotho yako yaikurukuru.

2 Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine ciani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliezere wa ku Damasiko?

3 Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga.

4 Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m'malo mwako; koma iye amene adzaturuka m'cuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m'malo mwako.

5 Ndipo anamturutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeuzako.

6 Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye cilungamo.

7 Ndipo anatikwaiye, Ine ndine Yehova amene ndinaturutsa iwe m'Uri wa kwa Akaldayo, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lako lako.

8 Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala colowa canga?

9 Ndipo anati kwa iye, Kanditengere Ine ng'ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda.

10 Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzace: koma mbalame sanazidula.

11 Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo.

12 Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikuru tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsya kwa mdima waukuru kunamgwera iye.

13 Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, nizidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;

14 ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pace adzaturuka ndi cuma cambiri.

15 Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m'mtendere; nudzaikidwa ndi ukalambawabwino.

16 Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wacinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.

17 Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng'anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto wapita pakati pa mabanduwo.

18 Tsiku lomwelo Yehova anapangana cipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pa nyanja ya Aigupto kufikira pa nyanja yaikuru, nyanja ya Firate:

19 Akeni ndi Akenizi, Akadimoni, ndi Ahiti, ndi Aperezi, ndi Arefai, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ajebusi.