1 Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Beteli nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.
2 Ndipo Yakobo anati kwa a banja lace, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Cotsani milungu yacilendo iri mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zobvala zanu:
3 tinyamuke, tikwere tinke ku Beteli: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandibvomereza tsiku la mabvuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo.
4 Ndipo anampatsa Yakobo milungu yacilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.
5 Ndipo anapita, ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera midzi yakuwazinga, ndipo sanalondola ana a Yakobo.
6 Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Beteli), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye.
7 Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, Dacha pamenepo El Beteli: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wace.
8 Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Beteli, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anacha dzina lace AlioniBakuti.
9 Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anacokera m'Padanaramu, namdalitsa iye.
10 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzachedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israyeli: ndipo anamucha dzina lace Israyeli.
11 Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, ucuruke; mwa iwe mudzaturuka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzaturuka m'cuuno mwako;
12 ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isake ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli.
13 Ndipo Mulungu anakwera kumcokera iye kumene ananena naye.
14 Ndipo Yakoboanaimiritsamwala pamalo pamene ananena ndi iye, coimiritsa camwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.
15 Ndipo anacha dzina lace la pamalo pamene Mulungu ananena ndi iye, Beteli.
16 Ndipo anacokera ku Beteli: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efrati: ndipo Rakele anabala nabvutidwa.
17 Ndipo panali pamene anabvutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna.
18 Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamucha dzina lace Benoni; koma atate wace anamucha Benjamini.
19 Ndipo anafa Rakele, naikidwa pa njira va ku Efrati (ndipo Betelehemu),
20 Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pace: umenewo ndi coimiritsa ca pa manda a Rakele kufikira lero.
21 Ndipo Israyeli anapita namanga hema wace patseri pa nsanja ya Edere.
22 Ndipo panali pamene Israyeli anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wace: ndipo Israyeli anamva.Ana amuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
23 ana amuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara;
24 ana amuna a Rakele: ndiwo Yosefe ndi Benjamini;
25 ana amuna a Biliha mdzakazi wace wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafitali;
26 ndipo ana amuna a Zilipa mdzakazi wace wa Leya: ndiwo Gadi ndi Aseri: amenewo ndi ana amuna a Yakobo amene anabala iye m'Padanaramu.
27 Ndipo Yakobo anafika kwa Isake atate wace ku Mamre, ku KiriyatiAriba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isake.
28 Ndipo masiku a Isake anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu.
29 Ndipo Isake anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wace, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ace amuna anamuika iye.