Genesis 34 BL92

Dina ndi a Sekemu

1 Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.

2 Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wace wamwamuna wa Hamori Mhivi, karonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa,

3 Ndipo mtima wace unakhumba Dina mwana wace wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.

4 Ndipo anati Sekemu kwa atate wace Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga.

5 Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wace wamkazi; ana ace amuna anali ndi zoweta zace kudambo: ndipo Yakobo anakhala cete mpaka anafika iwo.

6 Ndipo Hamori atate wace wa Sekemu anaturuka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye.

7 Ndipo pakumva ico ana ace amuna a Yakobo anabwera pocokera kudambo: amunawo ndipo anaphwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, cifukwa iyeyo anacita copusa coipira Israyeli pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndico cosayenera kucita.

8 Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wace.

9 Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi.

10 Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kucita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo.

11 Ndipo Sekemu anati kwa atate wace wa mkazi ndi kwa abale ace, Tipeze ufulu pamaso panu, cimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.

12 Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.

13 Ndipo ana ace amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wace monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,

14 nati kwa iwo, Sitingathe kucita ici, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; cifukwa kumeneko ndiko kuticepetsa ife.

15 Koma apa pokha tidzakubvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndi kudulidwa amuna onse;

16 pamenepo tidzakupatsani inu ana athu akazi, ndipo tidzadzitengera ana anu akazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi.

17 Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.

18 Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wace wa Hamori.

19 Ndipo mnyamatayo sanacedwa kucicita popeza anakondwera ndi mwana wace wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wace.

20 Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wace anafika ku cipata ca mudzi wao, nalankhulana ndi anthu a mudzi wao, kuti,

21 Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; cifukwa cace akhale m'dzikomo, acite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikololirilalikurulokwaniraiwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.

22 Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.

23 Kodi ng'ombe zao ndi cuma cao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tibvomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.

24 Ndipo onse amene anaturuka pa cipata ca mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wace Sekemu, nadulidwa amuna onse akuturuka pa cipata ca mudzi wao.

25 Ndipo panali tsiku lacitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ace a Dina, anatenga wina lupanga lace wina lace, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse.

26 Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wace ndi lupanga, naturutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nacoka naye.

27 Ndipo ana amuna a Yakobo anadzakwa ophedwa nafunkhamudzi cifukwa anamuipitsa mlongo wao.

28 Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi aburu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda;

29 ndi cuma cao conse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba.

30 Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwaodisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperezi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.

31 Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsamloogo wathu wadama?