Genesis 6 BL92

Kulowerera kwa mtundu wa anthu

1 Ndipo panali pamene anthu anayamba kucuruka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo,

2 kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.

3 Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, cifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ace adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri.

4 Pa dziko lapansi panali anthu akurukuru masiku omwewo ndiponso pambuyo pace, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.

5 Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukuru pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

6 Ndipo Yehova anamva cisoni cifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anabvutika m'mtima mwace.

7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva cisoni cifukwa ndapanga izo.

8 Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova.

9 Mibadwoya Nowandiiyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yace; Nowa anayendabe ndi Mulungu.

10 Ndipo Nowa anabala ana amuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.

11 Ndipo dziko lapansi linabvunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi ciwawa.

12 Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linabvunda; pakuti anthu onse anabvunditsa njira yao pa dziko lapansi.

Cigumula

13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Cimariziro cace ca anthu onse cafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi ciwawa cifukwa ca iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi.

14 Udzipangire wekha cingalawa ca mtengo wanjale; upangemo zipinda m'cingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja.

15 Kupanga kwace ndi kotere: m'litari mwace mwa cingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwace mikono makumi asanu, m'msinkhu mwace mikono makumi atatu.

16 Uike zenera m'ciogalawaco, ulimarize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pace: khomo la cingalawa uike m'mbali mwace; nucipange ndi nyumba yapansi, ndi yaciwiri, ndi yacitatu.

17 Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa cigumula ca madzi pa dziko lapansi, kuti cionooge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa.

18 Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'cingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe.

19 Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiri ziwiri za mtundu wao ulowetse m'cingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.

20 Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiri ziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo.

21 Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, oudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo.

22 Cotero anacita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anacita.