Genesis 13 BL92

Abramu ndi Loti alekana

1 Ndipo anakwera Abramu kucoka ku Aigupto, iye ndi mkazi wace, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera.

2 Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golidi,

3 Ndipo anankabe ulendowace kucokera ku dziko la kumwera kunka ku Beteli, kufikira kumalo kumene kunali hema wace poyamba paja, pakati pa Beteli ndi Ai;

4 kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova.

5 Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema.

6 Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: cifukwa kuti cuma cao cinali cambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.

7 Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperezi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo.

8 Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisacite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: cifukwa kuti ife ndife abale.

9 Dziko lonse siliri pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere.

10 Ndipo Loti anatukula maso ace nayang'ana cigwa conse ca Yordano kuti conseco cinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Aigupto pakunka ku Zoari.

11 Ndipo Loti anasankha cigwa conse ca Yordano; ndipo Loti anacoka ulendo wace kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzace.

12 Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'midzi ya m'cigwa, nasendeza hema wace kufikira ku Sodomu.

13 Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ocimwa kwambiri pamaso pa Yehova.

Mulungu alonjeza kwa Abramu kumpatsa Kanani

14 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwela, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo:

15 cifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.

16 Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga pfumbi lapansi: cotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga pfumbi lapansi, comweconso mbeu yako idzawerengedwa.

17 Tauka, nuyendeyendc m'dzikoli m'litari mwace ndi m'mimba mwace; cifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.

18 Ndipo Abramu anasuntha hema wace nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre, imene iri m'Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.