Genesis 4 BL92

Kaini ndi Abele. Kuphedwa koyamba

1 Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wace Hava: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.

2 Ndipo anabalanso mphwace Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.

3 Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova.

4 Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zace ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yace:

5 koma sanayang'anira Kaini ndi nsembe yace. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yace.

6 Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako?

7 Ukacita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kucita zabwino, ucimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwace, ndipo iwe udzamlamulira iye.

8 Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwace. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwace, namupha,

9 Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga?

10 Ndipo anati, Wacita ciani? Mau a mwazi wa mphwako andipfuulira Ine kunthaka.

11 Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, Imene inatsegula pakamwa pace kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako:

12 pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yace: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi.

13 Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukuru kosapiririka.

14 Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.

15 Ndipo Yehova anati kwa iye, Cifukwa cace ali yense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika icizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe ali yense akampeza.

Mbumba ya Kaini

16 Ndipo Kaini anaturuka pamaso pa Yehova, ndipo anakhalam'dziko la Nodi, kum'mawa kwace kwa Edene.

17 Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wace; ndipo anatenga pakati, nabala Enoke: ndipo anamanga mudzi, naucha dzina lace la mudziwo monga dzina la mwana wace, Enoke.

18 Kwa Enoke ndipo kunabadwa Irade; Irade ndipo anabala Mehuyaeli; Mehuyaeli ndipo anabala Metusaeli; Metusaeli ndipo anabala Lameke.

19 Ndipo Lameke anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lace la wina ndi Ada, dzina lace la mnzace ndi Zila.

20 Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe,

21 Ndi dzina la mphwace ndilo Yubala; iye ndiye atate wao wa iwo oyimba zeze ndi citoliro.

22 Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a citsulo; mlongo wace wa Tubala-Kaini ndi Nama.

23 Lameke ndipo anati kwa akazi ace:Tamvani mau anga, Ada ndi Zila;Inu akazi a Lameke, mverani kunena kwanga:Ndapha munthu wakundilasa ine,Ndapha mnyamata wakundiphweteka ine,

24 Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri,Koma Lameke makumi asanu ndi awiri.

Kubadwa kwa Seti

25 Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wace; ndipo anabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Seti: Cifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu yina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha,

26 Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwamwana wamwamuna: anamucha dzina lace Enosi: pomwepo anthu anayamba kuchula dzina la Yehova.