Genesis 31 BL92

1 Yakobo afuna kwao nathawa nazo zace, Ndipo anamva mau a ana ace a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye cuma ici conse.

2 Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekera iye monga kale.

3 Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe.

4 Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zace,

5 ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekera ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine.

6 Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu.

7 Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipilo anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andicitire ine coipa.

8 Akati cotero, Zamathotho-mathotho zidzakhala malipilo ako, zoweta zonse zinabala zamathotho-mathotho; ndipo akati iye cotere, Zamipyololo-mipyololo zidzakhala malipilo ako, ziweto zonse zinabala mipyololo-mipyololo.

9 Comweco Mulungu anazicotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine.

10 Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaanga-maanga.

11 Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano,

12 Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololo-mipyololo, amathotho-mathotho, ndi amaangamaanga: cifukwa ndaona zonse zimene Labani akucitira iwe.

13 Ine ndine Mulungu wa ku Beteli, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine cilumbiriro: tsopano uka, nucoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako.

14 Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tiri nalonso gawo kapena colowa m'nyumba ya atate wathu?

15 Kodi satiyesa ife alendo? cifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu.

16 Cifukwa kuti cuma conse Mulungu anacicotsa kwa atate wathu ndi cathu ndi ca ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, ucite.

17 Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ace ndi akazi ace pa ngamila;

18 ndipo ananka nazo zoweta zace zonse, ndi cuma cace conse anacisonkhanitsa, zoweta zace anaziona m'Padan-aramu, kuti anke kwa Isake atate wace ku dziko la Kanani.

19 Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zace: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wace.

20 Ndipo Yakobo anathawa kwa Labani Msuriyamobisika, m'mene sanamuuzeiye kuti analinkuthawa.

21 Ndipo anathawa iye ndi zonse anali nazo: ndipo anauka naoloka panyanja naloza nkhope yace iyaog'anire ku phiri la Gileadi.

Labani alondola wothawayo

22 Tsiku lacitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa.

23 Ndipo iye anatenga abale ace pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye pa phiri la Gileadi.

24 Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Msuriya usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa,

25 Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wace m'phirimo: ndipo Labani ndi abale ace anamanga m'phiri la Gileadi.

26 Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wacitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga akazi, monga mikoli ya lupanga.

27 Wathawanji iwe mobisika, ndi kundicokera kutseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze?

28 Ndipo sunandiloleza ine ndimpsompsone ana anga amuna ndi akazi? wapusa iwe pakucita cotero.

29 M'dzanja langa muli mphamvu yakucitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.

30 Tsono ungakhale ukadamuka cifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga?

31 Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Cifukwa ndinaopa: cifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako akazi.

32 Ali yense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi movo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako ziri ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.

33 Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze, Ndipo anaturuka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele.

34 Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa cokhalira ca ngamila, nakhala pamenepo, Ndipo Labani anafunafuna m'hema monse, koma sanawapeze.

35 Ndipo Rakele anati kwa atate wace, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; cifukwa zocitika pa akazi ziri pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.

36 Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndacimwa ciani? ucimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?

37 Pakuti wafunafuna monse ndiri nazo, kodi wapeza ciani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika naco apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.

38 Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.

39 Cimene cinazomoledwa ndi cirombo sindinacitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unacifuna, cingakhale cobedwa kapena pausiku kapena pausana.

40 Cotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku cisanu; tulo tanga tinacoka m'maso mwanga.

41 Ndinakhala cotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe cifukwa ca ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi cimodzi cifukwa ca zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.

42 Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isake zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandicotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi nchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.

Labani apangana ndi Yakobo

43 Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzacitira ine ciani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?

44 Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe.

45 Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa.

46 Ndipo Yakobo anati kwa abale ace, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo.

47 Ndipo Labani anacha pamenepo Yegara-sahaduta; koma Yakobo anacha Galeeda.

48 Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Cifukwa cace anacha dzina lace, Galeeda;

49 ndi Mizipa, cifukwa kuti anati, Yehova ayang'anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzace.

50 Ukasautsa ana anga akazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako.

51 Ndipo Labani anati kwa Yakobo. Taona muluwu, taona coimiritsaci, ndaciimiritsa pakati pathu.

52 Muluwu ndiwo mboni, coimiritsaci ndico mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa coimiritsaci kudza kwa ine kuti ticitirane zoipa,

53 Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wace Isake.

54 Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ace kuti adye cakudya; ndipo anadya cakudya, nagona paphiripo usiku wonse.

55 M'mamawa Labani anauka nampsompsona ana ace amuna ndi akazi, nawadalitsa: ndipo Labani anacoka, nabwera kumalo kwace.