Genesis 1 BL92

1 PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

2 Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unaliokufungatira pamwamba pa madzi.

3 Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.

4 Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabino: ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.

5 Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anaucha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.

6 Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pa madzi, lilekanitse madzi ndi madzi.

7 Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi analf pamwamba pa thambolo: ndipo kunatero.

8 Ndipo Mulungu analicha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku laciwiri.

9 Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.

10 Ndipo Mulungu adaucha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adaucha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

11 Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere maudzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wace, momwemo muli mbeu yace, pa dziko lapansi: ndipo kunatero.

12 Ndipo dziko lapansi linamera maudzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wace, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yace, monga mwa mtundu wace; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

13 Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacitatu.

14 Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;

15 zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi; ndipo kunatero.

16 Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikuru ziwiri; counikira cacikuru cakulamulira usana, counikira cacing'ono cakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.

17 Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi,

18 nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabino.

19 Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacinai.

20 Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zocuruka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga.

21 Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikuru ndi zoyendayenda zamoyo zakucuruka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wace: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

22 Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zicuruke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zicuruke pa dziko lapansi.

23 Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu.

24 Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.

25 Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wace, ndi zonse zakukwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.

Kulengedwa kwa munthu

26 Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

27 Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

28 Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

29 Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu liri pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli cipatso ca mtengo wakubala mbeu; cidzakhala cakudya ca inu:

30 ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale cakudya: ndipo kunatero.

31 Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu ndi cimodzi.