Genesis 37 BL92

Yosefe agulitsidwa ndi abale ace

1 Ndipo Yakobo anakhala m'dziko limene anakhalamo mlendo atate wace, m'dziko la Kanani.

2 Mibadwo ya Yakobo ndi iyi: Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ace; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wace; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wace mbiri yao yoipa.

3 Koma Israyeli anamkonda Yosefe koposa ana ace onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wace; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro.

4 Ndipo abale ace anaona kuti atate wace anamkonda iye koposa abale ace onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.

5 Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ace; ndipo anamuda iye koposa.

6 Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota:

7 pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima ciriri! ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga.

8 Abale ace ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? ndipo anamuda Iye koposa cifukwa ca maloto ace ndi mau ace.

9 Ndipo analotanso lata lina, nafotokozera abale ace, nati, Taonani, ndalotanso lata lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.

10 Ndipo iye anafotokozera atate wace ndi abale ace; ndipo atate wace anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi?

11 Ndipo abale ace anamcitira iye nsanje, koma atate wace anasunga mau amene m'mtima mwace.

12 Ndipo abale ace ananka kukaweta zoweta za atate wao m'Sekemu.

13 Ndipo Israyeli anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta m'Sekemu? tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano.

14 Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta ziri bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kucokera m'cigwa ca Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu.

15 Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m'thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna ciani?

16 Ndipo iye anati, Ndifuna abale anga. Undiuzetu kumene adyetsa zoweta.

17 Munthuyo ndipo anati, Anacoka pano; pakuti ndinamva alinkuti, Timuke ku Dotana. Yosefe ndipo anatsata abale ace, nawapeza ali ku Dotana.

18 Ndipo iwo anamuona iye ali patari, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye ciwembu kuti amuphe.

19 Ndipo anati wina ndi mnzace, Taonani, alinkudza mwini maloto uja.

20 Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi cirombo; ndipo tidzaona momwe adzacita maloto ace.

21 Ndipo Rubeni anamva nampulumutsa iye m'manja mwao; nati, Tisamuphe iye,

22 Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'cipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye ra'manja mwao, ambwezenso kwa atate wace.

23 Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ace, anambvula Yosefe malaya ace, malaya amwinjiro amene anabvala iye;

24 ndipo anamtenga iye, namponya m'dzenjemo; m'dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m'menemo.

25 Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye cakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismayeli anacokera ku Gileadi ndi ngamila zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi libano alinkumuka kutsikira nazo ku Aigupto.

26 Ndipo Yuda anati kwa abale ace, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wace?

27 Tiyeni timgulitse iye kwa Aismayeli, tisasamulire iye manja; cifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ace.

28 Ndipo ana pita pamenepo Amidyani a malonda: ndipo anamturutsa namkweza Yosefem'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismayeli ndi ndalama zasiliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Aigupto.

29 Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsaru yace.

30 Ndipo anabwera kwa abale ace, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti?

31 Ndipo anatenga malaya ace a Yosefe, napha tonde, nabvika malaya m'mwazi wace:

32 natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.

33 Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi cirombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.

34 Yakobo ndipo anang'amba malaya ace, nabvala ciguduli m'cuuno mwace namlirira mwana wace masiku ambiri.

35 Ndipo ana amuna ace onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndirinkulirabe. Atate wace ndipo anamlirira.

36 Amidyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Aigupto kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.