Genesis 9 BL92

Mulungu acita pangano ndi Nowa

1 Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ace, nati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi.

2 Kuopsya kwanu, ndi kucititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pa nsomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.

3 Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.

4 Koma nyama, m'mene muli moyo wace, ndiwo mwazi wace, musadye.

5 Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wace wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.

6 Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wace udzakhetsedwa: cifukwa m'cifanizo ca Mulungu Iye anampanga munthu.

7 Ndi inu, mubalane, mucuruke; muswane pa dziko lapansi, nimucuruke m'menemo.

8 Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ace pamodzi naye, kuti,

9 Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;

10 ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zoturuka m'cingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi,

11 Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamarizidwanso konse ndi madzi a cigumula; ndipo sikudzakhalanso konse cigumula cakuononga dziko lapansi.

12 Ndipo anati Mulungu, Ici ndici cizindikiro ca pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, ku mibadwo mibadwo;

13 ndiika Uta-wa-Leza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala cizindikiro ca pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.

14 Ndipo padzakhala popimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo;

15 ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene liri ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse cigumula cakuononga zamoyo zonse.

16 Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lacikhalire liri ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi.

17 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ici ndici cizindikiro ca pangano ndalikhazikitsa popaogana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.

18 Ndi ana amuna a Nowa amene anaturuka m'cingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wace wa Kanani.

19 Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.

Kuledzera kwa Nowa

20 Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa:

21 namwa vinyo wace, naledzera; ndipo anali wamarisece m'kati mwa bema wace.

22 Ndipo Hamu atate wace wa Kanani, anauona umarisece wa atate wace, nauza abale ace awiri amene anali kunja.

23 Semu ndi Yafeti ndipo anatenga copfunda, naciika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda cambuyo, napfunditsa umarisece wa atate wao: nkhope zao zinali cambuyo, osaona umarisece wa atate ao.

24 Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwace, nadziwa cimene anamcitira iye mwana wace wamng'ono.

25 Ndipo anati,Wotembereredwa ndi Kanani:Adzakhala kwa abale ace kapolo wa akapolo:

26 Ndipo anati:Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu;Kanani akhale kapolo wace.

27 Mulungu akuze Yafeti,Akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wace.

28 Ndipo Nowa anakhala ndi moyo cigumula citapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu.

29 Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.