Genesis 29 BL92

Yakobo akomana ndi Rakele

1 Ndipo Yakobo ananka ulendo wace, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa.

2 Ndipo anayang'ana, taonani, citsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pacitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa citsime unali waukuru.

3 Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa citsime pamalo pace.

4 Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? nati, Ndife a ku Harana.

5 Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wace wa Nahori? nati, Timdziwa.

6 Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wace wamkazi alinkudza nazo nkhosa.

7 Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni.

8 Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuucotsa pakamwa pa citsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa.

9 Ali cilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wace, cifukwa anaziweta.

10 Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wace wa amace, ndi nkhosa za Labani mlongo wace wa amace, Yakobo anayandikira nagubuduza kuucotsa mwala pacitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wace wa amace.

11 Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mau ace, nalira.

12 Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbalewace wa atate wace, kuti ndiye mwana wace wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wace.

Labani alandira Yakobo

13 Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wace, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwace. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.

14 Ndipo Labani anati kwa iye, Etu, iwe ndiwe pfupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi.

15 Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Cifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwacabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani?

16 Ndipo Labani anali ndi ana akazi awiri, dzina la wamkuru ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele.

17 Maso a Leya anali ofok a, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola.

18 Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.

19 Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine.

20 Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka cifukwa ca cikondi cimene anamkonda iye naco.

Leya ndi Rakele

21 Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse Ine mkazi wanga, cifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.

22 Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero.

23 Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wace wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo.

24 Ndipo Labani anampatsa mwana wace wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wace kuti akhale mdzakazi wa Leya.

25 Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Ciani wandicitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe cifukwa ca Rakele? wandinyenga ine bwanji?

26 Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng'ono asanapatse wamkuru.

27 Umarize sabata lace la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso cifukwa ca utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri.

28 Yakobo ndipo anacita cotero namariza sabata lace; ndipo Labani anampatsa iye Rakele mwana wace wamkazi kuti akwatire iyenso.

29 Ndipo Labani anampatsa mwana wace wamkazi Rakele Biliha mdzakazi wace kuti akhale mdzakazi wa Rakele.

30 Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso.

Ana a Yakobo

31 Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leva, anatsegula m'mimba mwace; koma Rakele anali wouma.

32 Ndipo Leyaanatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namucha dzina lace Rubeni; pakuti anati, Cifukwa kuti tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine.

33 Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Cifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamucha dzina lace Simeoni.

34 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine cifukwa ndambalira iye ana amuna atatu; cifukwa cace anamucha dzina lace Levi.

35 Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; cifukwa cace anamucha dzina lace Yuda; pamenepo analeka kubala.