1 Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Aigupto; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Maigupto, anamgula iye m'manja mwa Aismayeli amene anatsika naye kunka iumeneko.
2 Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyace M-aigupto.
3 Ndipo mbuyace anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lace zonse anazicita.
4 Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pace, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, naika m'manja mwace zonse anali nazo.
5 Ndipo panali ciyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, ndi pa zace zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto cifukwa ca Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zace zonse, m'nyumba ndi m'munda.
6 Ndipo iye anasiya zace zonse m'manja a Yosefe; osadziwa comwe anali naco, koma cakudya cimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.
7 Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyace anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.
8 Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyace, Taonani, mbuyanga sadziwa cimene ciri ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zace zonse m'manja anga;
9 mulibe wina m'nyumba wamkuru ndine; ndipo sanandikaniza ine kanthu, koma iwe, cifukwa kuti uli mkazi wace: nanga ndikacita coipa cacikuru ici bwanji ndi kucimwira Mulungu?
10 Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvera mkazi kugona naye kapena kukhala naye.
11 Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire nchito yace; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo.
12 Ndipo mkazi anagwira iye copfunda cace, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya copfunda cace m'dzanja lace nathawa, naturukira kubwalo.
13 Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti anasiya copfunda cace m'dzanja lace, nathawira kubwalo,
14 anaitana amuna a m'nyumba yace, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Mhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinapfuula ndi mau akuru:
15 ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kupfuula, iye anasiya copfunda cace kwa me nathawira kubwalo.
16 Ndipo anasunga copfunda cace cikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyace.
17 Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, nati, Analowa kwa ine kapolo wa Cihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine:
18 ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kupfuula, iye anasiya cobvala cace kwa ine, nathawira kunja.
19 Ndipo panali pamene mbuyace anamva mau a mkazi wace, amene ananena kwa iye, kuti, Coteroci anandicitira ine kapolo wako; kuti iye anapsya mtima.
20 Ndipo mbuyace wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo.
21 Koma Yehova anali ndi Yosefe namcitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang'anira kaidi.
22 Ndipo woyang'anira kaidi anapereka m'manja a Yosefe akaidi onse okhala m'kaidimo, ndipo zonse iwo anazicita m'menemo, iye ndiye wozicita.
23 Woyang'anira m'kaidi sanayang'anira kanthu kali konse kamene kanali m'manja a Yosefe, cifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazicita, Yehova anazipindulitsa.