Genesis 47 BL92

Yakobo aonetsedwa kwa Farao

1 Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao, ndi zonse ali nazo, anacokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m'dziko la Goseni.

2 Ndipo mwa abale ace anatengako anthu asanu, nawaonetsa iwo kwa Farao.

3 Ndipo Farao anati kwa abale ace, Nchito yanu njotani? ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu.

4 Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m'dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m'dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m'dziko la Goseni.

5 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Atate wako ndi abale ako afika kwa iwe;

6 dziko la Aigupto liri pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.

7 Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wace, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao.

8 Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati?

9 Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo angam'masikua ulendowao.

10 Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, naturuka pamaso pa Farao.

11 Ndipo Yosefe anakhazika atate wace ndi abale ace, napatsa iwo pokhala m'dziko la Aigupto, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramese, monga analamulira Farao.

12 Ndipo Yosefe anacereza atate wace ndi abale ace, ndi mbumba yonse ya atate wace ndi cakudya monga mwa mabanja ao.

Yosefe agulira Farao dziko la Aigupto

13 Ndipo munalibe cakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; cifukwa cace dziko la Aaigupto ndi dziko la Kanani unalefuka cifukwa ca njalayo.

14 Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama ku nyumba ya Farao.

15 Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, Aaigupto onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife cakudya; tiferenji pamaso panu? zatsirizika ndalama.

16 Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng'ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng'ombe zanu ngati ndalama zatsirizika.

17 Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo cakudya cosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu; ndipo anawadyetsa iwo ndi cakudya cosinthana ndi zoweta zao zonse caka cimeneco.

18 Citatha caka cimeneco, anadza kwa iye caka caciwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe oza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu;

19 tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? mutigule ife ndi dziko lathu ndi cakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja.

20 Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Aigupto, cifukwa Aaigupto anagulitsa yense munda wace, cifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao.

21 Tsono anthu, anasunthira iwo ku midzi kucokera kumphepete kwa malire a Aigupto kufikira kumphepete kwina kwace.

22 Koma dziko la ansembe lokha sanagule, cifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; cifukwa cace sanagulitsa dziko lao.

23 Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu sizi, mubzale m'dziko.

24 Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za cakudya canu, ndi ca ana anu ndi mabanja anu.

25 Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.

26 Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Aigupto kuukira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao.

27 Ndipo Israyeli anakhala m'dziko la Aigupto, m'dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m'menemo, nabalana nacuruka kwambiri.

28 Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Aigupto zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wace zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.

29 Ndipo nthawi inayandikira kuti Israyeli adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wace wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga, nundicitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m'Aigupto;

30 koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kuturuka m'dziko la Aigupto, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzacita monga mwanena.

31 Ndipo anati, Undilumbirire ine; namlumbirira iye. Ndipo Israyeli anawerama kumutu kwa kama.