Genesis 43 BL92

Abale a Yosefe atsikiranso ku Aigupto

1 Ndipo njala inakula m'dzikomo.

2 Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Aigupto atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife cakudya pang'ono.

3 Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, Simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.

4 Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu cakudya.

5 Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.

6 Ndipo Israyeli anati, Cifukwa ninji munandicitira ine coipa cotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?

7 Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?

8 Ndipo Yuda anati kwa atate wace Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.

9 Ine ndidzakhala cikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, cifukwa cace cidzakhala pa ine masiku onse:

10 pakuti tikadaleka kucedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.

11 Ndipo Israyeli atate wao anati kwa iwo, Ngati comweco tsopano citani ici: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta a mankhwala pang'ono, ndi uci pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;

12 nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanacita dala;

13 mutengenso mphwanu, nimuoyamuke, mupitenso kwa munthu uja:

14 Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu cifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.

Abalewo m'nyumba Ya Yosefe

15 Amunawo ndipo anatenga mphatso, natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Aigupto, naima pamaso pa Yosefe.

16 Ndipo pamene anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wace, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakoozere, cifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.

17 Munthuyo anacita monga anamuuza Yosefe, ndipo munthuyo analowa nao anthuwo m'nyumba ya Yosefe.

18 Anthuwo ndipo anaopa, cifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Cifukwa ca ndalama zila zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone cifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi aburu athu.

19 Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,

20 Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula cakudya:

21 ndipo panali pamene ife tinafika padgono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lace, ndalama zathu mkulemera kwace; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.

22 Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule cakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu.

23 Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu, ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu cum a m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawaturutsira Simeoni.

24 Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa aburu ao cakudya.

25 Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; cifukwa anamva kuti adzadya cakudya pamenepo.

26 Pamene Yosefe anadza kunyumba kwace, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.

27 Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? wokalamba uja amene nunanena uja: kodi alipo?

28 Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ili bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye.

29 Ndipo iye anatucula maso ace naona Benjamini mphwace, mwana wa amace, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akucitire we ufulu, mwana wanga.

30 Ndipo Yosefe anafulumira, cifukwa mtima wace unakhumbitsa mphwace, ndipo mafuna polirira; nalowa m'cipinda ace naliramo.

31 Ndipo anasamba ikhope yace, naturuka; ndipo anadziletsa, nati, Ikani cakudya.

32 Ndipo anamuikira iye cace pa yekha, ndi wo cao pa okha, ndi Aaigupto ikudya naye cao pa okha; cifukwa aigupto sanathei kudya cakudya pamodzi ndi Ahebri: cifukwa kucita comweco nkunyansira Aaigupto.

33 Ndipo anakhala pamaso pace, woyanba monga ukuru wace, ndi wanng'ono mensa ung'ono wace; ndipo mazizwa wina ndi wina.

34 Ndipo mawagawira mitanda ya patsogolo pace; koma mtanda wa Benjamini maposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.