1 Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi:
2 Esau anatenga akazi ace a ana akazi a m'Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Mhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibeoni Mhivi;
3 ndi Basemati mwana wamkazi wa lsmayeli, mlongo wace wa Nabayoti.
4 Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reueli;
5 ndipo Oholibama anabala Jeusi, ndi Jalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana amuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani.
6 Ndipo Esau anatenga akazi ace, ndi ana ace amuna, ndi ana ace akazi, ndi anthu onse a m'banja mwace, ndi ng'ombe zace, ndi zoweta zace, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patari ndi Yakobo mphwace.
7 Cifukwa cuma cao cinali cambiri cotero kuti sanakhoza kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira cifukwa ca ng'ombe zao.
8 Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu.
9 Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi:
10 amenewa ndi maina a ana amuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wace wa Esau, Reueli mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wace wa Esau.
11 Ndipo ana amuna a Elifazi ndiwo Temani, Omari, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi.
12 Ndipo Timna anali mkazi wace wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleki: amenewa ndi ana amuna a Ada mkazi wace wa Esau.
13 Ndi ana amuna a Reueli: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; amenewa ndi ana a Basemati mkazi wace wa Esau.
14 Ana amuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibeoni, mkazi wace wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Jeusi, ndi Jalamu, ndi Kora.
15 Amenewa ndi mafumu a ana amuna a Esau: ana amuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omari, mfumu Zefo, mfumu Kenazi,
16 mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleki: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana amuna a Ada.
17 Amenewa ndi ana amuna a Reueli mwana wamwamuna wa Esau: mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Sama, mfumu Miza; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Reueli m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana amuna a Basemati mkazi wace wa Esau.
18 Amenewa ndi ana amuna a Oholibama mkazi wace wa Esau; mfumu Jeusi, mfumu Jalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wace wa Esau.
19 Amenewa ndi ana amuna a Esau, amenewa ndi mafumu ao; yemweyo ndi Edomu.
20 Amenewa ndi ana amuna a Seiri Mhori, okhala m'dzikomo: Lotani ndi Sobala, ndi Zibeoni, ndi Ana,
21 ndi Disoni ndi Ezeri ndi Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, ana a Seiri, m'dziko la Edomu.
22 Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu: mlongo wace wa Lotani anali Timna.
23 Ana a Sobali ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebali, Sefo ndi Onamu.
24 Ana a Zibeoni ndi amenewa: Aia ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'cipululu, pakudyetsa aburu a Zibeoni atate wace.
25 Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.
26 Ana a Disoni ndi awa: Hemadani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerana.
27 Ana a Ezeri ndi awa: Biliha, ndi Zavani, ndi Akani.
28 Ana a Disoni ndi awa: Uzi ndi Arana.
29 Mafumu obadwa kwa Ahori: mfumu Lotani, mfumu Sobali, mfumu Zibeoni, mfumu Ana,
30 mfumu Disoni, mfumu Ezeri, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m'dziko la Seiri.
31 Amenewo ndi mafumu analamulira m'dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israyeli mfumu ali yense.
32 Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira m'Edomu, ndipo dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.
33 Ndipo Bela anamwalira, ndipo Jobabi mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozara analamulira m'malomwace.
34 Ndipo Jobabi anamwalira, ndipo Husami wa ku dziko la Atemani analamulira m'malo mwaceo
35 Ndipo Husami anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midyani m'dambo la Moabu, analamulira m'malo mwace: dzina la mudzi wace ndi Avita.
36 Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masereka analamulira m'malo mwace.
37 Ndipo Samila anamwalira, ndipo Sauli wa ku Rehoboti pambali pa Nyanja analamulira m'malo mwaceo
38 Ndipo Sauli anamwalira, ndipo Baal-hanani mwana wamwamuna wa Akibori analamulira m'malo mwace.
39 Ndipo Baal-hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m'malo mwace; dzina la mudzi wace ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wace ndi Mehetabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-zahabi.
40 Maina a mafumu obadwa kwa Esau, monga mabanja ao, monga malo ao, monga maina ao ndi awa: mfumu Timna, mfumu Aliva, mfumu Jeteti:
41 mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni;
42 mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibezari;
43 mfumu Magidieli, mfumu Iramu; amenewa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwao m'dziko lokhala laolao. Uyo ndiye Esau atate wao wa Aedomu.