Genesis 28 BL92

1 Ndipo Isake anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani.

2 Tauka, nupite ku Padanaramu, ku nyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana akazi a Labani mlongo wace wa amako.

3 Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akucurukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu:

4 akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.

5 Ndipo Isake anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wace wa Betuele Msuriya, mlongo wace wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau.

Yakobo apita ku Padanaramu

6 Ndipo anaona Esau kuti Isake anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko;

7 ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani; ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wace ndi amace, nanka ku Padanaramu;

8 ndipo Esau anaona kuti ana akazi a Kanani sanakondweretsa Isake atate wace:

9 ndipo ananka kwa Ismayeli, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismayeli mwana wa Abrahamu, mlongo wace wa Nebayoti akhalemkazi wace.

Loto la Yakobo ku Beteli

10 Ndipo Yakobo anacoka m'Beereseba, nanka ku Harana.

11 Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, cifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wace, nagona tulo kumeneko.

12 Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pace ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.

13 Taonani, Yehova anaima pamwamba pace, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isake; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa Iwe ndi mbeu zako;

14 mbeu zako zidzakhala monga pfumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

15 Taonani, Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; cifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditacita cimene ndanena nawe.

16 Ndipo Yakobo anauka m'tulo tace, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe.

17 Ndipo anaopa, nati, Poopsya pompano! pompano ndipo pa nyumba ya Mulunga, si penai, pompano ndipo pa cipata ca kumwamba.

18 Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pa mutu wace, nauimiritsa, nathira mafuta pamtu pace.

19 Ndipo anacha dzina la pamenepo Beteli; pakuyamba dzina lace la mudziwo ndi Luzi.

20 Yakobo ndipo analumbiracilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m'njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zobvalira za kubvala,

21 kuti ndibwerenso ku nyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga,

22 ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.