1 Abrahamu ndipo anacoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kedesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo m'Gerari.
2 Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wace, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleke mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara.
3 Koma Mulungu anadza kwa Abimeleke m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, cifukwa ca mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
4 Koma Abimeleke sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?
5 Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osacimwa ndacita ine ici.
6 Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, lode ndidziwa ine, kuti wacita ico ndi mtima wangwiro, ndipo lnenso ndinakuletsa iwe kuti usandicimwire ine: cifukwa cace sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.
7 Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wace; cifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.
8 Ndipo Abimeleke analawira m'mamawa, naitana anyamata ace onse, nanena zonse rimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri.
9 Ndipo Abimeleke anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Waticitira ife ciani iwe? Ndakucimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga ucimo waukuru? Wandicitira ine zosayenera kuzicita.
10 Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Unaona ciani iwe kuti wacita ici?
11 Ndipo Abrahamu anati, Cifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine cifukwa ca mkazi wanga.
12 Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.
13 Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ici ndico cokoma mtima udzandicitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, iye ndiye mlongo wanga.
14 Ndipo Abimeleke anatenga nkhosa ndi ng'ombe nd akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wace.
15 Ndipo Abimeleke anati, Taona dziko langa liri pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.
16 Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama za siliva mazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.
17 Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anaciritsa Abimeleke, ndi mkazi wace, ndi adzakazi ace; ndipo anabala ana.
18 Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m'nyumba ya Abimeleke, cifukwa ca Sara mkazi wace wa Abrahamu.