Genesis 19 BL92

Cionongeko ca Sodomu ndi Gomora

1 Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa cipata ca Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yace.

2 Ndipo anati, Taonanitu, ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, lai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.

3 Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwace; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda cotupitsa, ndipo anadya,

4 Koma asanagone, anthu a m'mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;

5 ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utiturutsire iwo kuti tiwadziwe.

6 Ndipo Loti anaturukira kwa iwo pakhomo, natseka cambuyo pakhomo pace.

7 Ndipo anati, Abale anga, musacitetu koipa kotere.

8 Taonanitu, ndiri ndi ana akazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwaturutsire iwo kwa inu, mucite nao comwe cikomera inu; koma anthu awa musawacitire iwo kanthu; cifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa cindwi langa,

9 Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakucitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe citseko.

10 Komo anthu aja anaturutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo,

11 Ndipo anacititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akuru, ndipo anabvutika kufufuza pakhomo.

12 Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi, ndi onse ali nao m'mudzi muno, uturuke nao m'malo muno:

13 popeza ife tidzaononga malo ano, cifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge.

14 Ndipo anaturuka Loti nanena nao akamwini ace amene anakwata ana ace akazi, nati, Taukani, turukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ace anamyesa wongoseka.

15 Pamene kunaca, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi.

16 Koma anacedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lace, ndi dzanja la mkazi wace ndi dzanja la ana ace akazi awiri; cifukwa ca kumcitira cifundo Yehova; ndipo anamturutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.

17 Ndipo panali pamene anawaturutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usaceuke, usakhale pacigwa pali ponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.

18 Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu;

19 taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza cifundo canu, cimene munandicitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti cingandipeze ine coipaco ndingafe:

20 taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli wong'ono; ndithawiretu kumeneko, suli wong'ono nanga? ndipo ndidzakhala ndi moyo.

21 Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikubvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mudzi uwu umene wandiuza.

22 Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kucita kanthu usadafike kumeneko. Cifukwa cace anacha dzina la mudziwo Zoari.

23 Ndipo dzuwa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zoari.

24 Ndipo Yehova anabvumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulfure ndi mota kuturuka kwa Mulungu kumwamba;

25 ndipo anaononga midziyo, ndi cigwa conse, ndi onse akukhala m'midzimo, ndi zimene zimera panthaka.

26 Koma mkazi wace anaceuka ali pambuyo pace pa Loti, nasanduka mwala wamcere.

27 Ndipo Abrahamu analawiram'mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova:

28 ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la cigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.

29 Ndipo panali pamene Mulungu anaononga midzi ya m'cigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, naturutsa Loti pakati pa cionongeko, pamene anaononga midzi m'mene anakhalamo Loti.

Gwero La Amon; ndi Moabu

30 Ndipo Loti anabwera kuturuka m'Zoari nakhala m'phiri ndi ana akazi awiri pamodzi naye: cifukwa anaopa kukhala m'Zoari, ndipo anakhata m'phanga, iye ndi ana ace akazi.

31 Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe pa dziko lapansi mwamona amene adzalowa kwa ife monga amacita pa dziko lonse lapansi:

32 tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu.

33 Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wace; ndipo sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka,

34 Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu.

35 Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwa pomwe anagona ndi pomwe anauka.

36 Ndipo ana akazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao.

37 Woyamba ndipo anabala mwana wamwamona, namcha dzina lace. Moabu; yemweyo ndi atate wa Amoabu kufikira lero.

38 Wamng'ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namcha dzina lace Benammi; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.