1 Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima panyanja.
2 Ndipo, taonani, zinaturuka m'nyanja ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango.
3 Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinaturuka m'nyanjamo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphepete mwa nyanja.
4 Ndipo ng'ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka.
5 Ndipo anagona nalotanso kaciwiri: ndipo taonani, ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino.
6 Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao.
7 Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota.
8 Ndipo panali m'mamawa mtima wace unabvutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m'Aigupto, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lace; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
9 Pamenepo wopereka cikho wamkuru anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zocimwa zanga lero.
10 Farao anakwiya ndi anyamata ace, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkuru:
11 ndipo tinalota loto usiku umodzi ine ndi iye; tinalota munthu yense monga mwa kumasulira kwa loto lace.
12 Ndipo panali ndi ife mnyamata, Mhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga mwa loto lace anatimasulira.
13 Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudacitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampacika.
14 Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamturutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, napindula malaya ace, nalowa kwa Farao.
15 Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.
16 Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
17 Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa nyanja;
18 ndipo taona, zinaturuka m'nyanjamo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango;
19 ndipo, taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinaturuka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Aigupto;
20 ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa,
21 Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba.
22 Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino;
23 ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao;
24 ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine.
25 Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao liri limodzi: cimene Mulungu ati acite wammasulira Farao.
26 Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri: loto liri limodzi.
27 Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinaturuka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.
28 Ici ndi cinthu cimene ndinena kwa Farao: cimene Mulungu ati acite wasonyeza kwa Farao.
29 Taonani, zidzafika zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka cakudya m'dziko lonse la Aigupto;
30 ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zocuruka zonsezo m'dziko la Aigupto; ndipo njala idzapululutsa dziko;
31 ndipo zocuruka sizidzazindikirika cifukwa ca njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzabvuta.
32 Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, cifukwa cinthu ciri cokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kucicita.
33 Tsopano, Farao afunefune'munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Aigupto.
34 Farao acite cotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Aigupto m'zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka dzinthu.
35 Iwo asonkhanitse cakudya conse ca zaka zabwino izo zirinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale cakudya m'midzi, namsunge.
36 Ndipocakudyacocidzakhalam'dziko cosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Aigupto; kuti dziko lisanonongedwe ndi njala.
37 Ndipo cinthuco cinali cabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ace.
38 Ndipo Farao anati kwa anyamata ace, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwace?
39 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.
40 Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wacifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.
41 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Taona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Aigupto.
42 Ndipo Farao anacotsa mphete yosindikizira yace pa dzanja lace, naibveka pa dzanja la Yosefe, nambveka iye ndi zobvalira zabafuta, naika unyolo wagolidi pakhosi pace;
43 ndipo anamkweza iye m'gareta wace waciwiri amene anali naye: ndipo anapfuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Aigupto,
44 Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu ali yense adzatukula dzanja lace kapena mwendo wace m'dziko lonse la Aigupto.
45 Ndipo Farao anamucha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anaturuka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Aigupto.
46 Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aigupto, Ndipo Yosefe anaturuka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Aigupto,
47 Ndipo zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri.
48 Ndipo anasonkhanitsa cakudya conse ca zaka zisanu ndi ziwiri cimene cinali m'dziko la Aigupto, nasunga cakudyaco m'midzi; cakudya ca m'minda, yozinga midzi yonse, anacisunga m'menemo.
49 Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mcenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; cifukwa anali wosawerengeka.
50 Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana amuna awiri, cisanafike caka ca njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Porifera wansembe wa Oni anambalira iye.
51 Ndipo Yosefe anamucha dzina la woyamba Manase, cifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zobvuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga.
52 Ndipo dzina la waciwiri anamucha Efraimu: cifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.
53 Ndipo zaka zakucuruka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Aigupto, zinatha.
54 Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Aigupto munali cakudya.
55 Ndipo pamene dziko lonse la Aigupto linali ndi njala, anthu anapfuulira Farao awapatse cakudya; ndipo Farao anati kwa Aaigupto onse, Pitani kwa Yosefe: cimene iye anena kwa inu citani.
56 Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aaigupto: ndipo njala inakula m'dziko la Aigupto.
57 Ndipo maiko onse anafika ku Aigupto kudzagula tirigu kwa Yosefe: cifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.